1
Genesis 50:20
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri.
አወዳድር
{{ጥቅስ}} ያስሱ
2
Genesis 50:19
Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu?
3
Genesis 50:21
Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.
4
Genesis 50:17
‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.
5
Genesis 50:24
Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.”
6
Genesis 50:25
Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”
7
Genesis 50:26
Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.
ቤት
መጽሐፍ ቅዱስ
እቅዶች
ቪዲዮዎች