LUKA 20:46-47
LUKA 20:46-47 BLP-2018
Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando; amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero aatali; amenewo adzalandira kulanga koposa.