1
LUKA 17:19
Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.
Qhathanisa
Hlola LUKA 17:19
2
LUKA 17:4
Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.
Hlola LUKA 17:4
3
LUKA 17:15-16
Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau aakulu; ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.
Hlola LUKA 17:15-16
4
LUKA 17:3
Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire.
Hlola LUKA 17:3
5
LUKA 17:17
Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwe khumi? Koma ali kuti asanu ndi anai aja?
Hlola LUKA 17:17
6
LUKA 17:6
Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.
Hlola LUKA 17:6
7
LUKA 17:33
Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga.
Hlola LUKA 17:33
8
LUKA 17:1-2
Ndipo anati kwa ophunzira ake, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo. Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwake ndi kuponyedwa iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.
Hlola LUKA 17:1-2
9
LUKA 17:26-27
Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu. Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo.
Hlola LUKA 17:26-27
Ikhaya
IBhayibheli
Amapulani
Amavidiyo