Logo ng YouVersion
Hanapin ang Icon

Ntc. 12

12
Herode apha Yakobe nkuponya Petro m'ndende
1Pafupi ngati nthaŵi imeneyo mfumu Herode adagwira ena a mu Mpingo kuti aŵazunze. 2Adalamula kuti Yakobe, mbale wake wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. 3Ndipo ataona kuti zimenezi zidakondweretsa Ayuda, adapitiriza ndithu nkugwiranso Petro. Zimenezi zidachitika pa masiku a Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa.#12.3: Chikondwerero cha mikate yosafufumitsa: Onani pa Eks. 12.15. 4#Eks. 12.1-27Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita. 5Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza.
Mngelo atulutsa Petro m'ndende
6Usiku woti m'maŵa mwake Herode azenga mlandu wake, Petro adaagona pakati pa asilikali aŵiri. Anali womangidwa ndi maunyolo aŵiri, ndipo pakhomo pa ndende panali alonda ena. 7Mwadzidzidzi kudafika mngelo wa Ambuye ndipo kuŵala koti mbee kudaunika m'chipindamo. Mngeloyo adagunduza Petro m'nthitimu kuti amdzutse, ndipo adati, “Dzuka msanga!” Pompo maunyolo aja adakolopoka m'manja mwake. 8Kenaka mngelo uja adamuuza kuti, “Vala lamba wako ndi nsapato zako.” Petro atachita zimenezi mngelo uja adamuuzanso kuti, “Fundira mwinjiro wako, unditsate.” 9Apo Petro adatuluka namtsata, osazindikira kuti zimene mngelo ankachitazo nzoona. Ankangoyesa kuti akuwona zinthu m'masomphenya chabe. 10Onsewo adapitirira gulu loyamba la asilikali aja, kenaka lachiŵiri, mpaka kukafika pa chitseko chachitsulo cha pa chipata choloŵera mu mzinda. Chitsekocho chidangodzitsekukira chokha, iwowo nkutuluka. Adayenda ndithu mu mseu wina wamumzindamo. Atafika polekezera pake mngelo uja adamchokera. 11Pamenepo Petro adadzidzimuka nati, “Tsopano ndikudziŵadi kuti Ambuye anatuma mngelo wao ndipo andipulumutsa kwa Herode, ndi ku zoipa zonse zimene Ayuda ankayembekeza kuti zidzandichitikira.”
12Atazindikira zimenezi, adapita kunyumba kwa Maria, amai ake a Yohane wotchedwanso Marko. Anthu ambiri anali atasonkhana kumeneko akupemphera. 13Pamene Petro adagogoda pa chitseko chapakhomo, mtsikana wina, dzina lake Roda, adabwera kuti amtsekulire. 14Atazindikira liwu lake kuti ndi la Petro, adakondwa kwambiri, kotero kuti sadatsekule chitsekocho, koma adathamangiranso m'kati nakawuza ena aja kuti, “Petro ali pakhomopa!” 15Anthuwo adati, “Wapenga iwe!” Koma iye adalimbikira kuti nzoonadi. Apo iwo adati, “Ndi mngelo wake#12.15: Mngelo wake: Ayuda ankakhulupirira kuti munthu aliyense ali ndi mngelo womtchinjiriza. ameneyo.” 16Koma Petro ankangogogodabe. Pamene adamtsekulira nkuwona kuti ndiyedi, adangoti kakasi. 17Petro adakweza dzanja kuti iwo akhale chete, naŵafotokozera m'mene Ambuye adaamtulutsira m'ndende muja. Ndipo adati, “Mumuuze Yakobe ndi abale ena aja zimenezi.” Pamenepo iye adatuluka napita kwina.
18Kutacha, asilikali aja adasokonezeka kwabasi nati, “Petro wapita kuti?” 19Herode adamufunafuna, koma osampeza. Adaŵazenga mlandu alonda aja, nalamula kuti aphedwe. Pambuyo pake Herode adachoka ku Yudeya kupita ku Kesareya, nakakhala kumeneko.
Za imfa ya Herode
20 # 2Am. 9.5-28 Herode adaaŵakwiyira anthu a ku Tiro ndi a ku Sidoni. Tsono anthuwo adadza pamodzi kwa iye. Adaayamba akopa Blasito, kapitao wa ku nyumba ya mfumu kenaka nkukapempha mtendere, chifukwa chakudya cha m'dziko laolo chinkachokera m'dziko la mfumuyo.
21Adapangana tsiku, ndipo pa tsikulo Herode adavala zovala zake zachifumu nkukhala pa mpando wake wachifumu, nayamba kuŵalankhula anthu aja. 22Anthuwo adanena mokweza mau kuti, “Ameneŵa ndi mau a mulungu, osati a munthu ai.” 23Pompo mngelo wa Ambuye, adamkantha Herodeyo chifukwa sadapereke ulemu kwa Mulungu. Mphutsi zidamudya ndipo adafa.
24Koma mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira.
25Tsono Barnabasi ndi Saulo atakwaniritsa zimene adaaŵatumira ku Yerusalemu, adabwerako. Adatengako Yohane wotchedwa Marko uja.

Kasalukuyang Napili:

Ntc. 12: BLY-DC

Haylayt

Ibahagi

Kopyahin

None

Gusto mo bang ma-save ang iyong mga hinaylayt sa lahat ng iyong device? Mag-sign up o mag-sign in