Ntc. 11:23-24
Ntc. 11:23-24 BLY-DC
Pamene iye adafika kumeneko nkuwona m'mene Mulungu adaŵadalitsira, adakondwa, nalimbikitsa onsewo kuti atsimikize mtima kukhala okhulupirika kwa Ambuye. Barnabasiyo anali munthu wolungama, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro. Choncho anthu ambirimbiri adakopeka nadzipereka kwa Ambuye.