Pamenepo Ananiya adanyamuka nakaloŵa m'nyumbamo. Adamsanjika manja Sauloyo nati, “Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene adakuwonekera pa njira imene wadzera ija, andituma. Akufuna kuti upenyenso, ndipo udzazidwe ndi Mzimu Woyera.” Pompo m'maso mwake mudachoka zinthu zonga mamba a nsomba, ndipo adayambanso kupenya. Adaimirira nabatizidwa