Tsono ngati Mulungu adaŵapatsa iwowo mphatso yomweyo imene adapatsa ifeyo pamene tidakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, nanga ine ndine yani kuti ndikadatha kumletsa Mulungu?”
Pamene otsutsana naye aja adamva zimenezi, adaleka mitsutsoyo. Adatamanda Mulungu adati, “Kodi kani! Ndiye kuti Mulungu wapatsadi ndi akunja omwe mwai woti atembenuke mtima ndi kulandira moyo!”