1
YOHANE 1:12
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake
ஒப்பீடு
YOHANE 1:12 ஆராயுங்கள்
2
YOHANE 1:1
Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.
YOHANE 1:1 ஆராயுங்கள்
3
YOHANE 1:5
Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira.
YOHANE 1:5 ஆராயுங்கள்
4
YOHANE 1:14
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
YOHANE 1:14 ஆராயுங்கள்
5
YOHANE 1:3-4
Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa. Mwa Iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.
YOHANE 1:3-4 ஆராயுங்கள்
6
YOHANE 1:29
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!
YOHANE 1:29 ஆராயுங்கள்
7
YOHANE 1:10-11
Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye. Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.
YOHANE 1:10-11 ஆராயுங்கள்
8
YOHANE 1:9
Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.
YOHANE 1:9 ஆராயுங்கள்
9
YOHANE 1:17
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
YOHANE 1:17 ஆராயுங்கள்
முகப்பு
வேதாகமம்
வாசிப்புத் திட்டங்கள்
காணொளிகள்