Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi adachimwa ndani kuti munthu ameneyu abadwe wakhungu? Adachimwa ndi iyeyu kapena makolo ake?” Yesu adati, “Sikuti iyeyu adachimwa kapena makolo ake ai. Koma adabadwa wakhungu kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iye.