1
Gen. 15:6
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama.
Compare
Explore Gen. 15:6
2
Gen. 15:1
Zitatha izi, Chauta adaonekera Abramu m'masomphenya namuuza kuti, “Usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.”
Explore Gen. 15:1
3
Gen. 15:5
Pomwepo Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “Tayang'ana kuthamboku, ndipo uŵerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.”
Explore Gen. 15:5
4
Gen. 15:4
Tsono Chauta adamuuza kuti, “Uyu sadzalandira chuma chako kukhala choloŵa chake. Yemwe adzalandire chuma chakochi ndi mwana wako weniweni.”
Explore Gen. 15:4
5
Gen. 15:13
Chauta adamuuza kuti, “Udziŵe ndithu kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni. Zidzakhala akapolo kumeneko, ndipo zidzazunzika zaka zokwanira 400.
Explore Gen. 15:13
6
Gen. 15:2
Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, ine ndilibe ana. Tsono mungathe bwanji kundipatsa mphotho? Woloŵa m'malo mwanga ndi Eliyezere wa ku Damasikoyu.
Explore Gen. 15:2
7
Gen. 15:18
Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
Explore Gen. 15:18
8
Gen. 15:16
Patapita mibadwo inai, zidzukulu zakozo zidzabwereranso, chifukwa sindidzaŵathamangitsa Aamori mpaka kuipa kwao kutafika pachimake penipeni kuti adzalangidwe.”
Explore Gen. 15:16
ಮುಖಪುಟ
ಬೈಬಲ್
ಯೋಜನೆಗಳು
ವೀಡಿಯೊಗಳು