1
Marko 10:45
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”
ប្រៀបធៀប
រុករក Marko 10:45
2
Marko 10:27
Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”
រុករក Marko 10:27
3
Marko 10:52
Yesu anati, “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!” Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.
រុករក Marko 10:52
4
Marko 10:9
Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”
រុករក Marko 10:9
5
Marko 10:21
Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.”
រុករក Marko 10:21
6
Marko 10:51
Yesu anamufunsa kuti, “Ukufuna ndikuchitire chiyani?” Wosaonayo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndikufuna ndione.”
រុករក Marko 10:51
7
Marko 10:43
Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira
រុករក Marko 10:43
8
Marko 10:15
Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.”
រុករក Marko 10:15
9
Marko 10:31
Koma ambiri amene ndi woyambirira adzakhala omalizira, ndipo omalizira adzakhala oyambirira.”
រុករក Marko 10:31
10
Marko 10:6-8
Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’ ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi.
រុករក Marko 10:6-8
ទំព័រដើម
ព្រះគម្ពីរ
គម្រោងអាន
វីដេអូ