Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako. Achite mdulidwe ndithu mwana wamwamuna aliyense, mbadwa ngakhale kapolo wochita kugula ndi ndalama, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro pa thupi lanu cha pangano langa lamuyaya.