1
Gen. 13:15
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Ndidzakupatsa dziko lonse limene ukuliwonalo, iweyo pamodzi ndi zidzukulu zako. Ndipo lidzakhala lako mpaka muyaya.
Összehasonlít
Fedezd fel: Gen. 13:15
2
Gen. 13:14
Loti atachoka, Chauta adauza Abramu kuti, “Uyang'ane bwino kumpoto, kumwera, kuvuma ndi kuzambwe.
Fedezd fel: Gen. 13:14
3
Gen. 13:16
Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kudzaziŵerenga. Yekhayo amene angaŵerenge fumbi la pa dziko lapansi, ndiye adzathe kuŵerenga zidzukulu zakozo.
Fedezd fel: Gen. 13:16
4
Gen. 13:8
Tsono Abramu adauza Loti kuti, “Ifetu ndife abale, choncho pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, ndipo abusa ako sayenera kumakangana ndi abusa anga.
Fedezd fel: Gen. 13:8
5
Gen. 13:18
Motero Abramu adazula hema lake, nakakhala patsinde pa mitengo ya thundu ya ku Mamure, imene ili ku Hebroni. Ndipo kumeneko adamangira Chauta guwa.
Fedezd fel: Gen. 13:18
6
Gen. 13:10
Motero Loti atayang'anayang'ana, adaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yordani mpaka ku Zowari chili ndi madzi ambiri. Chigwacho chinali ngati munda wa Chauta kapenanso ngati dziko la Ejipito. Nthaŵi imeneyi nkuti Chauta asanaononge mizinda ya Sodomu ndi Gomora.
Fedezd fel: Gen. 13:10
Kezdőoldal
Biblia
Olvasótervek
Videók