1
Yoh. 1:12
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.
השווה
חקרו Yoh. 1:12
2
Yoh. 1:1
Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu.
חקרו Yoh. 1:1
3
Yoh. 1:5
Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako.
חקרו Yoh. 1:5
4
Yoh. 1:14
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
חקרו Yoh. 1:14
5
Yoh. 1:3-4
Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. Mwa Iyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuŵala kounikira anthu.
חקרו Yoh. 1:3-4
6
Yoh. 1:29
M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
חקרו Yoh. 1:29
7
Yoh. 1:10-11
Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire.
חקרו Yoh. 1:10-11
8
Yoh. 1:9
Kuŵala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano.
חקרו Yoh. 1:9
9
Yoh. 1:17
Paja Mulungu adatipatsa Malamulo ake kudzera mwa Mose, koma kudzera mwa Yesu Khristu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake.
חקרו Yoh. 1:17
בית
כתבי הקודש
תכניות
קטעי וידאו