LUKA 17:1-2
LUKA 17:1-2 BLP-2018
Ndipo anati kwa ophunzira ake, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo. Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwake ndi kuponyedwa iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.