Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, adzakhala angaanga okondedwa pa tsiku limene ndidzalikonza. Ndidzaŵachitira chifundo monga m'mene munthu amachitira ndi mwana wake womtumikira. Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu abwino ndi anthu oipa, pakati pa anthu otumikira Mulungu ndi osamtumikira.”