1
MACHITIDWE A ATUMWI 2:38
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Vergleichen
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:38
2
MACHITIDWE A ATUMWI 2:42
Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:42
3
MACHITIDWE A ATUMWI 2:4
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:4
4
MACHITIDWE A ATUMWI 2:2-4
Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:2-4
5
MACHITIDWE A ATUMWI 2:46-47
Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m'Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:46-47
6
MACHITIDWE A ATUMWI 2:17
Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:17
7
MACHITIDWE A ATUMWI 2:44-45
Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:44-45
8
MACHITIDWE A ATUMWI 2:21
Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:21
9
MACHITIDWE A ATUMWI 2:20
dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera.
Studiere MACHITIDWE A ATUMWI 2:20
Home
Bibel
Lesepläne
Videos