Logo YouVersion
Ikona vyhledávání

GENESIS 8:21-22

GENESIS 8:21-22 BLPB2014

Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo. Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.