Yoh. 21:15-17
Yoh. 21:15-17 BLY-DC
Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m'mene amandikondera aŵa?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.” Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.” Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga.