YouVersion Logo
Search Icon

LUKA 16

16
Fanizo la kapitao wonyenga
1Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake. 2Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao. 3Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. 4Ndidziwa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene ananditulutsa muukapitao, anthu akandilandire kunyumba kwao. 5Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wake, nanena kwa woyamba, Unakongola chiyani kwa mbuye wanga? 6Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu. 7Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Madengu a tirigu zana. Iye ananena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu. 8#Aef. 5.8Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika. 9Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha. 10#Mat. 25.21Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu. 11Chifukwa chake ngati simunakhala okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? 12Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni? 13#Mat. 6.24Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Za mphamvu ya chilamulo
14Koma Afarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka. 15Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu. 16#Mat. 11.12-13Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kulowamo. 17#Yes. 40.8; Mat. 5.18Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono kachilamulo kagwe nkwapatali. 18#Mat. 5.32; 1Ako. 7.10-15Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.
Fanizo la mwini chuma ndi Lazaro waumphawi
19Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; 20ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, 21ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. 22Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. 23Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. 24Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. 25#Luk. 6.24Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. 26Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. 27Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; 28pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. 29#Yoh. 5.39, 45Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. 30Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. 31#Yoh. 12.10-11Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.

Currently Selected:

LUKA 16: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in