EKSODO 15:23-25
EKSODO 15:23-25 BLPB2014
Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara. Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani? Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa