MACHITIDWE A ATUMWI 8:29-31
MACHITIDWE A ATUMWI 8:29-31 BLPB2014
Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu. Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga? Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.