1 SAMUELE 21:12-13
1 SAMUELE 21:12-13 BLPB2014
Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati. Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.