Mateyu 7:1-3
Mateyu 7:1-3 CCL
“Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe. Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo. “Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako?