Luka 3:21-22
Luka 3:21-22 CCL
Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”