Luka 20:46-47
Luka 20:46-47 CCL
“Chenjerani ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo amakonda kuyenda atavala mikanjo ndipo amakonda kulonjeredwa mʼmisika ndipo amakhala mʼmipando yofunika mʼmasunagoge ndi mʼmalo aulemu mʼmaphwando. Amawadyera akazi amasiye chuma chawo ndi kuchita mapemphero aatali kuti awaone. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”