Luka 17:1-2
Luka 17:1-2 CCL
Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo. Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa.