Genesis 49:24-25
Genesis 49:24-25 CCL
Koma uta wake sunagwedezeke, ndi manja ake amphamvu aja analimbika, chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo, chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli. Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza; chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa ndi mvula yochokera kumwamba, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.