Genesis 18:23-24
Genesis 18:23-24 CCL
Kenaka Abrahamu anasendera kufupi ndi Iye nati, “Kodi mudzawonongera kumodzi wolungama ndi woyipa? Nanga bwanji patakhala anthu makumi asanu olungama mu mzindamo? Kodi mudzawonongadi onse osausiyako mzindawo chifukwa cha anthu makumi asanu olungama omwe ali mʼmenemo?