Machitidwe a Atumwi 11:17-18
Machitidwe a Atumwi 11:17-18 CCL
Tsono ngati Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyo imene anatipatsa ife, amene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti nditsutsane ndi Mulungu?” Iwo atamva zimenezi analibenso chonena ndipo anayamika Mulungu nati, “Potero Mulungu wapatsa anthu a mitundu ina mwayi wotembenuka mtima ndi kulandira moyo.”