1
Lk. 17:19
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Kenaka Yesu adauza munthuyo kuti, “Nyamuka, pita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”
Compare
Explore Lk. 17:19
2
Lk. 17:4
Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”
Explore Lk. 17:4
3
Lk. 17:15-16
Tsono mmodzi mwa iwo, ataona kuti wachira, adabwerera nayamba kuyamika Mulungu mokweza mau. Adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu, namthokoza. Koma munthuyo anali Msamariya.
Explore Lk. 17:15-16
4
Lk. 17:3
Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire.
Explore Lk. 17:3
5
Lk. 17:17
Apo Yesu adati, “Kodi achira aja si khumi? Nanga asanu ndi anai ena aja ali kuti?
Explore Lk. 17:17
6
Lk. 17:6
Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”
Explore Lk. 17:6
7
Lk. 17:33
Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga.
Explore Lk. 17:33
8
Lk. 17:1-2
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Zochimwitsa anthu sizingalephere kuwoneka, koma tsoka kwa munthu wobwera nazoyo. Kukadakhala kwabwino kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamponya m'nyanja, kupambana kuti achimwitse mmodzi mwa ana ang'onoang'onoŵa.
Explore Lk. 17:1-2
9
Lk. 17:26-27
“Monga momwe zidaachitikira pa nthaŵi ya Nowa, zidzateronso pa nthaŵi ya Mwana wa Munthu. Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse.
Explore Lk. 17:26-27
Home
Bible
Plans
Videos