1
Gen. 22:14
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.”
Compare
Explore Gen. 22:14
2
Gen. 22:2
Mulungu adati, “Tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza.”
Explore Gen. 22:2
3
Gen. 22:12
“Usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziŵa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
Explore Gen. 22:12
4
Gen. 22:8
Abrahamu adamuyankha kuti, “Mwana wanga, Mulungu akatipatsa mwanawankhosayo.” Choncho onse aŵiri adapitiriza ulendo wao limodzi.
Explore Gen. 22:8
5
Gen. 22:17-18
Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.’ ”
Explore Gen. 22:17-18
6
Gen. 22:1
Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee Ambuye.”
Explore Gen. 22:1
7
Gen. 22:11
Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati
Explore Gen. 22:11
8
Gen. 22:15-16
Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiŵiri kuchokera kumwamba, adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezi, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja.
Explore Gen. 22:15-16
9
Gen. 22:9
Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo.
Explore Gen. 22:9
Home
Bible
Plans
Videos