Mulungu adamuyankha m'maloto momwemo kuti, “Inde ndikudziŵa kuti iwe udachita zimenezi popanda mtima wako kukutsutsa. Choncho ndidakuletsa ndine kuti usandichimwire pakumkhudza mkaziyo. Koma tsopano, umpereke mkazi ameneyu kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti usafe. Koma ukapanda kumpereka, ndikukuchenjezeratu kuti udzafa ndithu, iweyo ndi banja lako lonse.”