Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera