Ndipo anati kwa ana a Israele, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani? Pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israele anaoloka Yordani uyu pouma. Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordani pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anachitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka