Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo. Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.