1
EKSODO 5:1
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Compare
Explore EKSODO 5:1
2
EKSODO 5:23
Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditsa anthu anu konse.
Explore EKSODO 5:23
3
EKSODO 5:22
Pamenepo Mose anabwerera namka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? Mwandituma bwanji?
Explore EKSODO 5:22
4
EKSODO 5:2
Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.
Explore EKSODO 5:2
5
EKSODO 5:8-9
Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita chilezi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu. Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza.
Explore EKSODO 5:8-9
Home
Bible
Plans
Videos