nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita. Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makhumi