Pofika tsono kulowa kwake kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Mordekai, amene adadzitengera akhale mwana wake, kuti alowe kwa mfumu, sanafune kanthu koma zonena Hegai mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.