1
MACHITIDWE A ATUMWI 1:8
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.
Compare
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 1:8
2
MACHITIDWE A ATUMWI 1:7
Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wake wa Iye yekha.
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 1:7
3
MACHITIDWE A ATUMWI 1:4-5
ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine; pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 1:4-5
4
MACHITIDWE A ATUMWI 1:3
kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 1:3
5
MACHITIDWE A ATUMWI 1:9
Ndipo m'mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao.
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 1:9
6
MACHITIDWE A ATUMWI 1:10-11
Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao; amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.
Explore MACHITIDWE A ATUMWI 1:10-11
Home
Bible
Plans
Videos