1
Marko 4:39-40
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata. Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”
Compare
Explore Marko 4:39-40
2
Marko 4:41
Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”
Explore Marko 4:41
3
Marko 4:38
Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”
Explore Marko 4:38
4
Marko 4:24
Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri.
Explore Marko 4:24
5
Marko 4:26-27
Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira.
Explore Marko 4:26-27
6
Marko 4:23
Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”
Explore Marko 4:23
Home
Bible
Plans
Videos