1
Marko 11:24
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.
Compare
Explore Marko 11:24
2
Marko 11:23
Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo.
Explore Marko 11:23
3
Marko 11:25
Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.”
Explore Marko 11:25
4
Marko 11:22
Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.
Explore Marko 11:22
5
Marko 11:17
Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ”
Explore Marko 11:17
6
Marko 11:9
Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti, “Hosana! “Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!”
Explore Marko 11:9
7
Marko 11:10
“Odala ndi ufumu umene ukubwera wa abambo athu Davide!” “Hosana Mmwambamwamba!”
Explore Marko 11:10
Home
Bible
Plans
Videos