Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano. Pakuti kwalembedwa,
“Adzalamulira angelo ake za iwe
kuti akutchinjirize mosamala;
ndipo adzakunyamula ndi manja awo,
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.”
Yesu anayankha kuti, “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”