Ngati wina adziyesa kanthu pamene iyeyo sali kanthu konse, akudzinamiza yekha. Munthu aliyense aziyesa yekha ntchito zake mmene zilili. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, iyeyo asadzifanizire ndi munthu wina wake, pakuti aliyense ayenera kusenza katundu wake.